Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalicho.
Eksodo 37:21 - Buku Lopatulika ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m'mwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m'mwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Panali nkhunje imodzi pansi pa magulu atatu a nthambi zija, zitapatulidwa ziŵiriziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mphukira yoyamba inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Mphukira yachitatu inali mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zinali nthambi zisanu ndi imodzi |
Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalicho.
pakhale mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalicho.
Ndipo pa choikaponyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;
Mitu yao ndi mphanda zao zinatuluka m'mwemo; chonsechi chinali chosulika pamodzi cha golide woona.