Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Eksodo 37:20 - Buku Lopatulika Ndipo pa choikaponyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pa choikapo nyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa thunthu lake la choikaponyalecho panali zikho zinai zonga maluŵa amtowo okhala ndi nkhunje zake ndi maluŵa ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa choyikapo nyalecho panali zikho zinayi zokhala ngati maluwa amtowo, mphukira ndi maluwa ake. |
Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalicho.
Ndipo pa choikaponyali chomwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;
pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyali.
ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m'mwemo.
inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona nthyole ya katungurume.
Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, n'kutulutsa timaani, ndi kuchita maluwa, n'kubereka akatungurume.