ndipo m'mbali zake mutuluke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikaponyalicho zituluke m'mbali yake ina, ndi mphanda zitatu za choikaponyalicho zituluke m'mbali inzake.
Eksodo 37:18 - Buku Lopatulika ndi m'mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikaponyali zotuluka m'mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikaponyali zotuluka m'mbali yake ina; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi m'mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake ina; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mbali zake adapanga nthambi zisanu ndi imodzi, zitatu pa mbali iliyonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼmbali mwake munali mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. |
ndipo m'mbali zake mutuluke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikaponyalicho zituluke m'mbali yake ina, ndi mphanda zitatu za choikaponyalicho zituluke m'mbali inzake.
Ndipo anapanga choikaponyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikaponyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo;
pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyali.
Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.