Eksodo 37:17 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga choikaponyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikaponyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo;
Onani mutuwo
Ndipo anapanga choikapo nyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikapo nyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo;
Onani mutuwo
Pambuyo pake adapanga choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zinali zagolide, ndipo zonse zinali zosula ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, adazipangira kumodzi ndi choikaponyalecho.
Onani mutuwo
Iwo anapanga choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zinasulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zinapangidwa kumodzi.
Onani mutuwo