nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova analamula ichitike.
Eksodo 36:6 - Buku Lopatulika Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mu chigono chonse, ndi kuti, Asaonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa chigono chonse, ndi kuti, Asaonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Mose adalamula anthu m'mahema monse kuti, “Mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense asaperekenso zopereka zomangira malo opatulika.” Motero anthu adaleka kubwera ndi zopereka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, |
nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova analamula ichitike.