Momwemo Solomoni anakuta m'kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide.
Eksodo 36:34 - Buku Lopatulika Ndipo anakuta matabwa ndi golide, napanga mphete zao zagolide zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakuta matabwa ndi golide, napanga mphete zao zagolide zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mafulemu onsewo adaŵakuta ndi golide, ndipo adamangapo mphete zagolide zopisiramo mitanda ija, imene adaikutanso ndi golide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anakuta maferemuwo ndi golide ndiponso anapanga mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso anayikuta ndi golide. |
Momwemo Solomoni anakuta m'kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide.
Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.