Ndipo azipanga likasa la mtengo wakasiya: utali wake mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwake mkono ndi hafu, msinkhu wake mkono ndi hafu.
Eksodo 36:20 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga matabwa a chihema, oimirika, a mtengo wakasiya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga matabwa a Kachisi, oimirika, a mtengo wakasiya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adapanga mafulemu a chihemacho ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anapanga maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. |
Ndipo azipanga likasa la mtengo wakasiya: utali wake mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwake mkono ndi hafu, msinkhu wake mkono ndi hafu.
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake.
Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu.
Ndipo Israele anakhala mu Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Mowabu;
Potero ndinapanga likasa la mtengo wakasiya, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m'phirimo, magome awiri ali m'manja mwanga.