ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Eksodo 36:19 - Buku Lopatulika Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adapanga chophimbira china chofiira cha zikopa za nkhosa zamphongo. Potsiriza adapanganso chophimbira china cha zikopa zofeŵa, nkuchiika pamwamba pa zophimba zina zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anapanga chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake anapanganso chophimbira china cha zikopa za akatumbu. |
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pake.
Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.