Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.
Eksodo 36:18 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adapanga ngoŵe zokoŵera zokwanira makumi asanu zamkuŵa zolumikizira pamodzi nsalu ziŵirizo, kuti apange chinsalu chimodzi chophimbira chihema. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anapanga ngowe 50 zamkuwa zolowetsa mu zokolowekazo ndipo anaphatikiza nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. |
Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.
Ndipo anapanga magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china.
Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake.