Ndipo anaomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; anaomba nsalu zophimba khumi ndi imodzi.
Eksodo 36:15 - Buku Lopatulika Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'litali mwa nsalu iliyonse munali mamita 14, ndipo muufupi mwake munali masentimita 183. Zonsezo zinali zofanana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nsalu zonse khumi ndi imodzi zinali zofanana. Mulitali mwake munali mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake munali mamita awiri. |
Ndipo anaomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; anaomba nsalu zophimba khumi ndi imodzi.