Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.
Eksodo 36:13 - Buku Lopatulika Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo chihema chinakhala chimodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo Kachisi anakhala mmodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adapanga ngoŵe zokoŵera zagolide makumi asanu, nalumikiza nsalu zazikulu ziŵirizo ndi ngoŵezo. Pamenepo chihema cha Chauta chidakhala chimodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi. |
Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.
Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.