Eksodo 34:32 - Buku Lopatulika Ndipo atatero, ana onse a Israele anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atatero, ana onse a Israele anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Aisraele onse adasendera pafupi, ndipo Mose adaŵapatsa malamulo onse amene Chauta adaamuuza ku phiri la Sinai lija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Aisraeli onse anamuyandikira, ndipo anawapatsa malamulo onse omwe Yehova anamupatsa pa Phiri la Sinai. |
Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.
Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao.
Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova analamula, kuti muwachite.
kuti mukumbukire ndi kuchita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;
Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Khristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo;