Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
Eksodo 34:31 - Buku Lopatulika Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Mose adaŵaitana, ndipo Aroni pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele aja atabwera kwa iye, Moseyo adayamba kulankhula nawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Mose anawayitana. Kotero Aaroni ndi atsogoleri onse a gululo anabwera kwa iye, ndipo anawayankhula. |
Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.
Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.
Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzake, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.
Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.
Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israele anaona Mose, taonani, khungu la nkhope yake linanyezimira; ndipo anaopa kumyandikiza.
Ndipo atatero, ana onse a Israele anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai.