Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.
Eksodo 34:25 - Buku Lopatulika Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero cha Paska asaisiye kufikira m'mawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero cha Paska asaisiye kufikira m'mawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Musapereke buledi wofufumitsa pamene mukupereka kwa Ine magazi a nsembe yanga. Nyama iliyonse yophera nsembe ya Paska, musaisunge mpaka m'maŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa. |
Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.
Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa.
Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wa chotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.
Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi.
Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi.
Kunena za nyama ya nsembe yolemekeza ya nsembe zoyamika zake, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa.
Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska.
Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.
Ndipo m'malire mwanu monse musaoneke chotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m'mawa.