Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 34:22 - Buku Lopatulika

Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Muzichita chikondwerero cha masabata, ndi chikondwerero cha kukolola tirigu woyambirira, ndi chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pake pa chaka.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Muzichita Chikondwerero cha Masabata, chifukwa ndi chikondwerero cha tirigu woyambirira kucha, ndiponso ndi chikondwerero cha kututa zokolola pakutha pa chaka.

Onani mutuwo



Eksodo 34:22
13 Mawu Ofanana  

monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka: pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.


Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka.


ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.


Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize paguwa la nsembe zichite fungo lokoma.


Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wansembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu;


Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri pali chikondwerero cha Misasa ya Yehova, masiku asanu ndi awiri.


Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.


Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira.


Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.


Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kusenga tirigu wachilili.