ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
Eksodo 34:19 - Buku Lopatulika Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwana wamphongo aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi wa zoŵeta yemwe, ndiye kuti ng'ombe ndi nkhosa zanu zomwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi ziweto zoyamba kubadwa zazimuna kuchokera ku ngʼombe kapena nkhosa. |
ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse Ine.
Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.
(monga mwalembedwa m'chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye)