koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;
Eksodo 34:17 - Buku Lopatulika Usadzipangire milungu yoyenga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usadzipangire milungu yoyenga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Musadzipangire milungu yosungunula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Musadzipangire milungu yosungunula. |
koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;
Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko.
wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.
Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lake losemasema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya mwa iwo.
Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.
Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:
Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.
Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko;
Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi.