Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.
Eksodo 33:7 - Buku Lopatulika Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose ankatenga chihema chija ndi kukachimanga kunja kwake kwa mahema, chapatali ndithu. Tsono adachitcha chihemacho dzina loti, “Chihema chamsonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Chauta ankatuluka kumahemako, napita ku chihema chamsonkhanocho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa. |
Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.
Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.
Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.
Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho.
koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.
Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.
Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.