Eksodo 33:23 - Buku Lopatulika ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzaona m'mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzaona m'mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka ndichotsa dzanja langa, ndipo undiwona kumsana, koma nkhope yanga suiwona ai.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka ine ndidzachotsa dzanja langa ndipo iwe udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sidzaoneka.” |
Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?
Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.
amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.