Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.
Eksodo 33:17 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ichi chomwe wanenachi ndidzachita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ichi chomwe wanenachi ndidzachita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adauza Moseyo kuti, “Ndidzachita monga wanena, chifukwa ndakukomera mtima, ndipo ndikukudziŵa bwino.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzachita zimene iwe wandipempha chifukwa Ine ndikukondwera nawe, ndikukudziwa bwino lomwe.” |
Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.
taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;
Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mzinda uwu umene wandiuza.
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitse amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga.
ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.
Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.
Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani. Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso.
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.