Eksodo 33:15 - Buku Lopatulika Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kuchokera kuno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kuchokera kuno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Mose adauza Chauta kuti, “Mukapanda kupita nafe limodzi, musatilole kuti tichoke pano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mose anati kwa Yehova, “Ngati inu simupita nafe, musatitumize kuti tipite, kutichotsa pano. |
Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.
Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.