Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 32:27 - Buku Lopatulika

Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m'chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m'chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

ndipo Mose adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Aliyense mwa inu atenge lupanga, ndipo mupite ku mahema ndi kuloŵa m'zipata zonse. Aliyense mwa inu akaphe mbale wake kapena bwenzi lake kapena mnansi.’ ”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, ‘Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’ ”

Onani mutuwo



Eksodo 32:27
12 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumzinda wa nyumba ya Baala.


Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana aamuna onse a Levi anasonkhana kwa iye.


Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu.


Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wake wamwamuna, ndi mdani wa mbale wake; kuti akudalitseni lero lino.


Nati kwa enawo, ndilikumva ine, Pitani pakati pa mzinda kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musachite chifundo;


Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori.


Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukuchetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.


Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;