Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse.
Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine mu Yuda ndi mu Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.
Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.
Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.