ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
Eksodo 31:13 - Buku Lopatulika Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uza Aisraele kuti, ‘Muzisunga Sabata, tsiku langa lopumula, chifukwa ndilo chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi inu ndi zidzukulu zanu, choonetsa kuti Ine ndine Chauta, amene ndimakuyeretsani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani. |
ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga kumwamba ndi dziko lapansi m'masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu.
Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi, amene asunga Sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lake osachita nalo choipa chilichonse.
musatulutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire ntchito ili onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;
Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.
Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pazikondwerero zanga zonse zoikika; napatulikitse masabata anga.
Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira Yehova Sabata.
Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;
Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?
Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu: