Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo mu Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya.
Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.