Eksodo 31:11 - Buku Lopatulika ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma, zonsezo zokhalira malo oyera. Adzapange zinthu zonsezi monga ndakulamulira iwe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.” |
Pamenepo anachita Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.
Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.