zovala za kutumikira nazo m'malo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakugwira nazo ntchito ya nsembe.
Eksodo 31:10 - Buku Lopatulika ndi zovala zotumikira nazo, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakuchita nazo ntchito ya nsembe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi zovala zotumikira nazo, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakuchita nazo ntchito ya nsembe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa zovala zopatulika za wansembe Aroni ndi za ana ake, zomavala pa nthaŵi imene akutumikira, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe, |
zovala za kutumikira nazo m'malo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakugwira nazo ntchito ya nsembe.
Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.