Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova analamula, kuti muwachite.
Eksodo 31:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Chauta adapitirira kuuza Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anati kwa Mose, |
Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova analamula, kuti muwachite.
Ndipo Mose anati kwa ana a Israele, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;
Pamenepo anachita Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.
Ndipo Bezalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, anapanga zonse zimene Yehova adauza Mose.
Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.