Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.
Eksodo 30:35 - Buku Lopatulika ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosakaniza mwa machitidwe a wosakaniza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosanganiza mwa machitidwe a wosanganiza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uphatikize pamodzi zonsezi, ndipo upange lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athiremo mchere, ndipo akhale woyera ndi wopatulika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uziphatikize pamodzi zonsezi ndi kupanga lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athire mchere ndipo akhale woyera ndi wopatulika. |
Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.
Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.
Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.
ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osakanizika monga mwa machitidwe a wosakaniza; akhale mafuta odzoza opatulika.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi lubani loona; miyeso yofanana;
nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.
Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.
Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makala amoto, kuwachotsa paguwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ake odzala ndi chofukiza chopera cha fungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsalu yotchinga;
Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wa chipangano cha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere.
Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.