Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Eksodo 30:33 - Buku Lopatulika Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu aliyense amene adzapange mafuta ena ofanafana nawo, kapena kudzozera munthu aliyense amene sali wansembe, adzamchotsa pakati pa anthu anzake.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wina aliyense amene adzapanga mafuta wonunkhira wofanana nawo kapena kudzozera mafutawa munthu wamba osati wansembe ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.” |
Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.
Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.
Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi lubani loona; miyeso yofanana;
Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m'mwemo, munthu ameneyo achotsedwe mwa anthu a mtundu wake.
Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzachotsedwa.
osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake;
osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wao.
koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake.
Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakamvula, anavula kasupe wake, ndi iye mwini anavula kasupe wa nthenda yake; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.
Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.
Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.
Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.
Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lake; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yake ikhale pa iye.
Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.
Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.