Eksodo 30:31 - Buku Lopatulika Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aisraele onse udzaŵauze kuti, ‘Ameneŵa ndiwo adzakhale mafuta anga oyera odzozera pa mibadwo yanu yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono awuze a Israeli kuti, mafuta wodzozera awa adzakhala wopatulika mpaka muyaya. |
Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.
Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.
Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.
Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung'amba zovala zake.