Eksodo 30:26 - Buku Lopatulika Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Udzadzoze chihema chamsonkhanocho ndi mafuta amenewo. Udzadzozenso bokosi lachipangano, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono uwagwiritse ntchito podzoza tenti ya msonkhano, Bokosi la Chipangano, |
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali paphiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.
Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.
Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;
Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka chiperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera nacho chopereka chao paguwa la nsembelo.
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.
Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.