asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.
Eksodo 30:22 - Buku Lopatulika Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauzanso Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anati kwa Mose, |
asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.
Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,
ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zake, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pakhomo, pa khomo la chihema;
Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.
ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho;
Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa chihema chonse, ndi zonse zili m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zake.