Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, chifukwa anatambasulira likasa dzanja lake, nafa komweko pamaso pa Mulungu.
Eksodo 30:20 - Buku Lopatulika pakulowa iwo m'chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakulowa iwo m'chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akamaloŵa m'chihema chamsonkhano, kapena kuyandikira guwalo pa ntchito yao yautumiki, ndi kumapereka kwa Chauta chopereka chopsereza, sadzafa malinga akasamba ndi madzi amenewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene akulowa mu tenti ya msonkhano, iwo asambe madziwa kuti asafe. Ndiponso pamene akupita kukatumikira ku guwa lansembe ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Yehova, |
Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, chifukwa anatambasulira likasa dzanja lake, nafa komweko pamaso pa Mulungu.
Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.
Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.
asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.
Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi.
Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake.
Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.
Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.