Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
Eksodo 29:44 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake amuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chihema chamsonkhanocho ndidzachisandutsa kuti chikhale chopatulika, pamodzi ndi guwa lomwe. Ndipo Aroni ndidzampatula pamodzi ndi ana ake aamuna, kuti akhale ansembe anga onditumikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira. |
Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.
ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.
kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?