ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosakaniza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;
Eksodo 29:32 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mudengu, pa khomo la chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni ndi ana ake amuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mudengu, pa khomo la chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Aroni ndi ana akewo adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, pamodzi ndi buledi wam'lichero uja pakhomo pa chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaroni ndi ana ake adye nyama ya nkhosa yayimunayi pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu pa khomo la tenti ya msonkhano. |
ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosakaniza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;
Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.
Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.