Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira.
Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.