Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
Eksodo 29:16 - Buku Lopatulika Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza paguwa la nsembe pozungulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono uiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza pa mbali zonse za guwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza mbali zonse zaguwalo. |
Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m'ziwalo zake, ndi kutsuka matumbo ake, ndi miyendo yake, ndi kuziika pa ziwalo zake, ndi pamutu pake.
Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira paguwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.
Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.