Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 29:15 - Buku Lopatulika

Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Utenge imodzi mwa nkhosa ziŵiri zamphongo zija, ndipo Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Utenge nkhosa yayimuna imodzi ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake.

Onani mutuwo



Eksodo 29:15
7 Mawu Ofanana  

Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.


Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.


Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.


Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.