Eksodo 29:10 - Buku Lopatulika Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pambuyo pake ubwere ndi ng'ombe yamphongo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Tsono Aroni ndi ana ake asanjike manja ao pamutu pa ng'ombeyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ubwere ndi ngʼombe yayimuna pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo Aaroni ndi ana ake asanjike manja awo pamutu pake. |
Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.
Utatha kuliyeretsa upereke mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda chilema.
Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.
ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,
Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.
Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la chihema chokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.
Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.
Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.
Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi.
Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.