Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi.
Eksodo 28:37 - Buku Lopatulika Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ulimange ndi kamkuzi kobiriŵira pa nduŵira ya Aroni, ndipo likhale cha kutsogolo kwa nduŵirayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ulimange ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira ya Aaroni, ndipo duwalo likhale kutsogolo kwa nduwirayo. |
Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi.
Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.
Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israele azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.
Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.
Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo.
Nena ndi ana a Israele, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zovala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi.