Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 28:32 - Buku Lopatulika

Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pakati pake pa mkanjowo usiye chiboo chopisapo mutu. Chiboo chimenechi chikhale chosokerera mwamphamvu mozungulira monse, ngati khosi la malaya, kuti mkanjowu usang'ambike.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mkanjowo ukhala ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo pakhale chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike.

Onani mutuwo



Eksodo 28:32
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zachitsulo, ndi malaya achitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera.


Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.


Munthu akaiyamba ndi lupanga, ligoma; ngakhale nthungo, kapena muvi, kapena mkondo.


Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha.


Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;


ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang'ambike.


ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,