Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
Eksodo 28:29 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israele pa chapachifuwa cha chiweruzo pamtima pake, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale chikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israele pa chapachifuwa cha chiweruzo pamtima pake, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale chikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Aroni akamaloŵa m'malo opatulika, azivala chovala chapachifuwa cholembedwa maina onse a ana a Israele, kuti Chauta azidzaŵakumbukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pamene Aaroni akulowa kumalo opatulika azivala chovala chapachifuwa cha zoweruzira chija chimene chalembedwa mayina a ana a Israeli kuti Yehova awakumbukire nthawi zonse. |
Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi.
Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israele pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza.
Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.
Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova.
Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.