Eksodo 28:26 - Buku Lopatulika Ndipo upange mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pansonga zake ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake, m'katimo ku mbali ya kuefodi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo upange mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa nsonga zake ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake, m'katimo ku mbali ya kuefodi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upangenso mphete ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zam'munsi za chovala chapachifuwa, ku nsonga yake yam'kati, pafupi ndi chovala cha efodi chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. |
Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.
Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi.
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.