Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.
Eksodo 28:24 - Buku Lopatulika Numange maunyolo awiri opota agolide ku mphete ziwirizo pansonga pake pa chapachifuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Numange maunyolo awiri opota agolide ku mphete ziwirizo pa nsonga pake pa chapachifuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umange zingwe zagolide ziŵiri ku mphete ziŵirizo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Umangirire timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. |
Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.
M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo.
ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.
Nupangire pa chapachifuwa mphete ziwiri zagolide, ndi kuzika mphete ziwirizo pansonga zake ziwiri za chapachifuwa.
Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.