Eksodo 28:20 - Buku Lopatulika ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mzere wachinai pakhale miyala ya berili, onikisi ndi jasipere, ndipo zonsezo ziikidwe m'zoikamo zagolide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mzere wachinayi pakhale miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi uyiike mu zoyikamo zagolide. |
Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.
Manja ake akunga zing'anda zagolide zoikamo zonyezimira zoti biriwiri. Thupi lake likunga chopanga cha minyanga cholemberapo masafiro.
Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.
Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga ina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo.
thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji.
ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;
ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.