Eksodo 28:19 - Buku Lopatulika ndi mzere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mizere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mzere wachitatu pakhale miyala ya yasinti, agate ndi ametisiti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mzere wachitatu pakhale miyala ya opera, agate ndi ametisiti. |
ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao.
Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.