Eksodo 28:18 - Buku Lopatulika ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahaloni; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahaloni; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mzere wachiŵiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi daimondi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mzere wachiwiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; |
ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee.
Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba;
Manja ake akunga zing'anda zagolide zoikamo zonyezimira zoti biriwiri. Thupi lake likunga chopanga cha minyanga cholemberapo masafiro.
Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe ao.
Ndi pamwamba pathambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake.
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kuthambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a chifaniziro cha mpando wachifumu pamwamba pao.
Aramu anachita nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsalu yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.
Unali mu Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.
ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.