Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Eksodo 28:17 - Buku Lopatulika Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usokererepo mizere inai ya miyala. Pa mzere woyamba pakhale miyala ya rubi, topazi ndi garaneti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyikepo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rubi, topazi ndi berili. |
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Chikhale chaphwamphwa, chopindika, utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi.
Alipo golide ndi ngale zambiri; koma milomo yodziwa ndiyo chokometsera cha mtengo wapatali.
Omveka ake anakonzeka koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka, matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.
Unali mu Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.
Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.