Ndipo anaika gomelo m'chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga.
Eksodo 26:35 - Buku Lopatulika Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikaponyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya chihema; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikapo nyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tebulo lija uliike kunja kwa nsalu yochingayo. Choikaponyale chija uchiike chakumwera kwake kwa chihemacho, mopenyana ndi tebulolo, limene likhale mbali yakumpoto. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo. |
Ndipo anaika gomelo m'chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga.
Ndipo anaika choikaponyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.
Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.
Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.
Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.